💃🎤 Paroles de chanson Française et Internationnales 🎤💃
|
|
A B C D E F G H I J K L M N O P Q R S T U V W X Y Z 0 1 2 3 4 5 6 7 8 9
Titre : Malawi - Mlungu salitsani malawi
Mlungu dalitsani Malaŵi,
Mumsunge m´mtendere.
Gonjetsani adani onse,
Njala, nthenda, nsanje.
Lunzitsani mitima yathu,
Kuti tisaope.
Mdalitse Mtsogoleri nafe,
Ndi Mayi Malaŵi.
Malaŵi ndziko lokongola,
La chonde ndi ufulu,
Nyanja ndi mphepo ya m´mapiri,
Ndithudi tadala.
Zigwa, mapiri, nthaka, dzinthu,
N´mphatso zaulere.
Nkhalango, madambo abwino.
Ngwokoma Malaŵi.
O Ufulu tigwirizane,
Kukweza Malaŵi.
Ndi chikondi, khama, kumvera,
Timutumikire.
Pa nkhondo nkana pa mtendere,
Cholinga n´chimodzi.
Mayi, bambo, tidzipereke,
Pokweza Malaŵi.